Apolisi a ku Area 23 amanga mkazi wazaka 34, dzina lake Bernadetta Awali, chifukwa choti anawotcha mwamuna wake, Yamikani Jonasi, ndi madzi otentha pambuyo pa mkangano wokhudza kulemba mtsikana wantchito m'nyumba.
Malinga ndi apolisi, banjali lomwe lakhala pa ukwati kwa zaka zisanu ndi ziwiri, lidayamba kukangana pomwe Jonasi adanena kuti akufunika kulemba munthu wothandiza panyumba. Adanena kuti Awali akuvutika kusamalira banja Kamba koti amakhala otanganidwa ndikuchita malonda ake.
Komabe, Awali akuti anakana lingaliroli chifukwa cha mantha oti mwamuna wake angachite chikondi ndi mtsikana wothandizira ntchito nyumbayo. Mantha amenewa akuti amachokera m’mbiri ya ubale wawo, popeza Awali kale anali wogwira ntchito m'nyumba ya a Jonasi ndipo Jonasi adasiya mkazi wake wakale Kamba ka Awali.
Mkanganowu unakula kwambiri tsiku la ngoziyo, ndipo akuti Awali anayamba kumuvulaza mwamuna wake ziwalo zake zogonana kenako kumuwotcha ndi madzi otentha.
Jonasi wavutika kwambiri ndi moto womwe unamuwotcha ndipo akulandira chithandizo ku Kamuzu Central Hospital, komwe madokotala akuti ali pa ululu waukulu koma ali m’malo otetezeka.
Apolisi atsimikiza kuti Awali ali m’ndende ndipo adzazengedwa milandu akamaliza kafukufuku.
Mkazi wa ku Area 23 Wamangidwa Kamba Kovulaza Mwamuna Wake Ndi Madzi Otentha Poti Analemba Wantchito Wamkazi
Apolisi a ku Area 23 amanga mkazi wazaka 34, dzina lake Bernadetta Awali, chifukwa choti anawotcha mwamuna wake, Yamikani Jonasi, ndi madzi otentha pambuyo pa mkangano wokhudza kul...
By editor·April 8, 2026·2 min read
439

More in gossip
gossipeditor
Water Shortages, Blackouts Hit Tinubu’s Presidential Villa
Nigeria’s Presidential Villa in Abuja, the country’s seat of power, is reportedly experiencing water shortages and elect…
51 0
gossipeditor
BEDBUGS TAKE OVER NEW YORK 911 CENTRE, FORCE STAFF TO WORK FROM HOME
New York City, the city of skyscrapers, Wall Street and some of the world's most sophisticated emergency services, is re…
75 0
gossipeditor
Ultrarunner Ditches Nike Sponsorship for OnlyFans After Wikipedia Scandal
Famed ultrarunner Camille Herron has found an unexpected way to keep her running career financially afloat, and it appea…
83 0


