A polisi a m'boma la Nsanje akusunga amayi awiri powaganizira kuti anapha bambo wina wa dzaka 25. mu mudzi wa Nyale kwa Traditional Authority Mbenje.
Amayiwa omwe ndi Moreen Jambo, wa dzaka 18, ndi Modester Foster, wa dzaka 32, amachokera mmudzi wa Nyale ndipo akuganizilidwa kuti apha bambo Khefasi Liwichi, adzaka 25, omwe amachokera mmudzi wa Gamba kwa mfumu yayikulu Mbenje m'boma la Nsanje.
Utsiku wapa 31 October, bambo Khefasi adakangana kwambiri ndi mkazi wawo Moreen chifukwa adachoka pakhomopo tsiku lonse nkubwela mochedwa.
N'kanganowu udayambitsa ndewu ndipo Moreen adathawila kwa mayi ake omwe amakhala pafupi nawo. Bambo Khefasi powona izi sadayilole ndipo adapita kwa Apongozi awo konko kukayishosha bhawuthi.
Popeza Moreen ndi Mayake Modestor adali team imodzi, adamugwila mwamuna uja nkumukoka maliseche mpaka bamboyo kumwalira.
Atamutengera kuchipatala zinaziwika kuti bamboyi adamwalira kamba ka ululu womwe udaza kamba kotchosedwa maliseche.
Padakali pano amayi awiriwa akusungidwa mchitokosi cha apolisi pomwe akuyembekezera kukaonekera ku bwalo la milandu.
Nsanje Police Deputy PRO
, Constable Jabulani Ng’oma, wavomeleza za nkhani yi
APHA MWAMUNA WAKE POMUFINYA KUMOYO MOTHANDIZIDWA NDI MAYAKE
A polisi a m'boma la Nsanje akusunga amayi awiri powaganizira kuti anapha bambo wina wa dzaka 25. mu mudzi wa Nyale kwa Traditional Authority Mbenje. Amayiwa omwe ndi Moreen Jambo,...
By editor·April 8, 2026·2 min read
23


More in home
homeeditor
MV Chambo Tragedy on Lake Malawi Sparks Concern for Passengers
Sadness and concern have emerged following reports that MV Chambo exploded and sank on Lake Malawi, with the fate of pas…
12430 3
homeeditor
Meta AI model hacks external system during cybersecurity test
Meta has disclosed that one of its artificial intelligence models accessed the internet and hacked into an external comp…
2530 1
homeeditor
Parliament Passes Banking Amendment Bill to Strengthen Depositor Protection
Parliament has passed the Banking Amendment Bill, 2026, aimed at strengthening banking regulation, protecting depositors…
2090 1


